Voice of Islam Malawi ndi wayilesi ya Chisilamu yomwe cholinga chake ndi kufalitsa uthenga wa Qur’an ndi Sunnah, kupereka maphunziro achipembedzo, kulimbikitsa anthu pa zabwino, komanso kuthandiza Asilamu kumvetsetsa bwino chipembedzo chawo. Wayilesiyi imabweretsa mapulogalamu osiyanasiyana okhudza Aqeedah, Fiqh, Tafseer, Hadith, mbiri ya Asilamu, makhalidwe abwino, banja, maphunziro a achinyamata, komanso nkhani zofunika kwa anthu a mdera.
Voice of Islam Malawi imapereka mwayi kwa omvera kumvera ma Bayan, ma lecture, zokambirana ndi akatswiri a Chisilamu, mafunso ndi mayankho, komanso mapulogalamu ophunzitsa Qur’an ndi Sunnah. Cholinga chake ndi kuthandiza anthu kuphunzira, kukumbutsidwa, ndi kulimbikitsidwa kutsatira njira yolondola ya Chisilamu.